16/06/2026
Osewera kutsogolo wa timu ya Flames, Khuda 'Ikenna' Myaba yemwe pakadali pano alibe timu wati wakonzeka kuthandiza timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuyamba kuchita bwino mu ligi ya FDH Bank ya chaka chino.
"Ndamva zoti anawina ndikale IM AVAILABLE ine, FCB Nyasa Big Bullets bolani ndalama basi mwina mudalira ana aku reserve side ambiri akugona, " Myaba walemba izi pa tsamba lake la mchezo la Facebook Lachiwiri m'mawa.
M'masewero asanu ndi amodzi amu ligi ya FDH Bank, Bullets yapeza chipambano m'masewero awiri ndipo yafananitsa mphamvu m'masewero ake anayi.
📸 Social Media