15/08/2026
Brothers and sisters omwe muli ku South Africa….tagulani malo pa trading center iliyonse or mbali mwa nseu mumange ma shop.
Malo omanga ma shop sikuti amakhala aaakulu ayi.
Ma shop samafuna mpanda.
Enanso amatha kumanga without toilets zimakhala zatheka…apapa you can build a single smart toilet.
Shop simafuna zambiri ka rectangle basi.
Denga lake limakhala la straight osati kulipindapinda mkumakutheranso ndalama.
Tapangani izizi.
Ma shop akusowa kwambiri these days.
Ku Blantyre kuno ka shop kakang’ono unva 120pin.
Nde ukhale ndi ma shop four malo amodzi kungomanga midadada.
Ndalama yomwe ukhoza kuononga kumanga self contained house kuti uzilandirapo 250k pamwezi, the same money if you build five shops utha kumalandirapo more than 500k.
Zomabwera ku Malawi kuno mkungokhala kwa three days mkubwelera ku South Africa zimatanthauza kuti ulibe plan yeniyeni ku Malawi kuno.
Utakhala kuti wamanga ma shop awawa nde usunge imodzi ikhale yako ukabwera uzatsegule uzigulisamo mchape wako apapa ndekuti wamuposa ogwira ntchito m’boma.
Shop or patakhala popanda madzi nzabhobho….a single tap is enough.
Nyumbatu imafuna zambiri, ndalama zomwe zimalowa ku septic tank yokha ukhozatu kugulira malo ena.
Shop simafuna sink ayi.
Shop mpaka giza?
Shop palibe zoti ili khonde lakumaso ili khonde lakuseli ayi.
Kumanga shop is simple.
Taithamangeni.
Mukamayendayenda muzilimba mtima kuti Muli ndi podalira.
Business yamphanvu iyi that’s why mu Chitawiramu anthu aionelera akumangoboola mpanda kumangapo ka shop unva rent 200k.
Shop kungoika ma tiles ndi ceiling imakhala yakwera mtengo kuposa nyumba.
Zomagula malo kumudzi mkumangako nyumba nzabwino inde Koma vuto ndi loti mukabwera mumafuna mukhale mtown pomwe nyumba munamanga kumudzi koti olo rent singalowedwe.
Ngati ukufuna kumanga nyumba Umange malo oti rent ikhoza kuzatheka.
Read, think, act and repeat.
Kalowa nkhutu kayaza!
Nzeru mkupangwa!
Njuli Builders-Ma
+265 888 878 678
+265 995 690 336