23/08/2026
DID YOU KNOW?
KAPANGIDWE KA MBEYA
ZOFUNIKA
1. 10Kg ya Madeya, kapena utuchi(sawdust)
2. 20 kg ya Ndowe za mtundu uliwonse (zabwino ndizomwe zinaumila pa mthunzi)
3. 10 kg ya phulusa losefedwa bwino
4. 10 kg ya fertilizer: Gwiritsani ntchito NPK ngati mukupanga feteleza wothira koyamba (Basal), kapena Urea ngati mukupanga wa kachiwiri (Top dressing).
5. 5litres madzi/mkodzo: zabwino kugwilitsa ntchito nkodzo chifukwa mumapezeka nitrogen yemwe amapanga boost mbeya.
6. Thumba la 50kg: lomwe liri ndi pepala la plastic mkati mwake
NDONDOMEKO YAKAPANGIDWE KA MBEYA
1.Kusakaniza zipangizo zouma
▶️ Yalani pepala kapena chisaka choyera pamalo a mthunzi. Thirani deya, ndowe, phulusa ndi feteleza zimene munayeza zija ndikusakaniza mpaka zonse zisakanilane bwinobwino.
2. Kuthira Mkodzo
▶️ Thirani mkodzo wanu pang'ono-pang'ono mukumasakaniza. Osapanga zosakanizazo kukhala ngati matope.
▶️ Mkodzo uli ndi nitrogen wamphamvu kwambiri yemwe amathandiza kuti zinthuzi ziwole msanga. Chinyontho chimafunika kuti tizilombo tiyambe kugwira ntchito, koma madzi akachuluka kwambiri, mpweya umatha ndipo feteleza wanu amanunkha komanso kuonongeka.
3. Kulongedza m'Thumba
▶️ Khuthulirani zosakaniza m'thumba lija liri ndi plastic mkati.
▶️ Osathinikiza kapena kupondereza mukamalonga kuti zisaundane. Mangani kaye plastic yamkati kenako n'kumanga thumba lakunja bwinobwino.
▶️ Plastic amathandizira kuti feteleza asataye mpweya kapena michere yofunika (nitrogen gas) yomwe imatuluka chifukwa chakutentha.
✅️Ikitsani thumba lanu pamalo ozizira, a mthunzi kwa masiku 21 (masabata atatu). Thumba lidzatentha kwambiri mkati izi zimalora fertilizer yi aphye.
▶️ Kutenthaku kumaphanso tizilombo toyambitsa matenda komanso mbewu za namsongole zomwe zinali m'manyowa.
4. Kuyanika ndi Kusunga
▶️ Akatha matsiku 21, muzayanika fertilizer wanuyo pa mthunzi kwa masiku atatu mpaka asanu kuti awume bwinobwino. Kuyanika pa mnthunzi kuti michere isasungunuke nkoonongeka.
▶️ Mukatha, mukhoza kuwapakiranso m'masaka wamba n'kusunga m'khola kapena m'nyumba yosungiramo zinthu. Akhoza kukhala nthawi yaitali.
Note: sitikuletsa kugwilitsa ntchito inorganic fertilizer koma kulimbikitsa chabe kugwilitsa ntchito Mbeya yemwe ali ndi maubwinonso ochuluka.
Kukhala ndikuthekera m***a kuthira mbeya komanso fertilizer.
ZIKOMO